Welcome to dotSUB!
Any Video Any Language
Here you can view, upload, transcribe and translate any video into any language. To create your own subtitles, click the button below and register.
Enterprise Solutions
dotSUB's Enterprise Solutions are a cost-effective platform for managing high-quality subtitles at scale, deploying them to video players and mobile devices, and providing interactive transcripts for enhanced SEO.
Transcript for Edith Kaphuka - Ngwale Village, Malawi - Nyanja (Global Lives Project, 2007) ~19:02:00 - 19:17:01
Izizi zinali pamwamba, ndiye zangokhala ngati zangodutsidwa pangono. Iyayi, izizi zinali pansi. Zokupsyazo izizi izi, zokhala ngati zokomana ndangowumba nkuyikazo. -Ehe! -Eyetu! -Amangowumba nthawi yomweyo nkuyika? -Eetu zimawumira pompatu. -Uuhh. -1972. -Ndiye siziphwaphwathika? -Ayi. -Zimangopangika chidothidothi. -Akamayika njerwa yina pamwamba... Yina yabwafuka. A Felix abwera. Felix uja! Amene uja lachitatu lina lili lonse amawumba njerwa. Eeh ndimawapeza akuwumba njerwa. Amene uja samankhumbira anzake akuyimba? Ine ndimaona ngati amakhumbira. Aa! Kodi anasiyiranji? Chifukwa choti ankayenda ndi... Ndiye anazangoti angolowa yathuyi. Ali Ayango tiye tipange, choir. Ikhale kaya akuti Gold chani? Ku Golden City. -Choir imeneyo ndiye simandibebela. -Ya china Martha aja? -Nyimbo zake zi, kaya zitatu zitatu zokha. -Amangobweleza! -Eeh! -Mulungu sanalembe. Amayi... kukhala ngati kuti adalemba. Koma ndiye tinakuchedwa kutuluka. Kutuluka. Ku-tu-lu-kaa. -Ine nde tulo likubwera. -Inenso. Anzako ayamba ntchito. Chani? Aah! Ndimafuna ndizilotatu sitikubwera, aah! Ife tayamba kale kulotatu. Inde akuti chonchi... kuti chonchi. -Halleluyah! -Hosanna! Ine ngati ndayamba pano nde kuliri andiuze kuti nditembenukile uko! Nde ndinyangala bwanji? Olo ndimanyoza ineyo, ngati nditembenuketu ndi mwayi. Upitetu kumu... kumtunda, kumusi... Ukagona uyikeno mutu uko. Mukutero, koma kuti tiyeke mutuko, iih! Mayo! Ndiye tigona lero? Iiih! Tulo lolitchezekera man! Sumagona. Umangolota chimkango chikukugogometsa! Eeh! Hee, kuuzadzidzimuka tulo kutheratu... Ndikupenya chinyali. Ine zinandichitikirapo... Nena akuti chani? -Eeh! -Akunena ndani? Eeh! Nambotu yamasengotu. Titulukenso! Abale tikakweche mbale! Ine ndikali kugona, koma ndikunyangala. Taonani fumbi uku kuli bi! Apapa! Kodi ujeni nditembenukire uku ine ndiye sinditembenukira... Siya! Is very very very... Nditembenulira ukoko siziziwika. Koma apatsidwa mateche, makofi, machiani? Mambama! -Eya. -Apapa tilowe mubulangete ili. Koma apa timayenera kulipanga chonchi, ndimayesa ukuku ndikubweletsera lalikulu chonchi. Chonchi. Wawona, wawona? Ndiye kumunsiku... Zingakhaleso bo! -Komatu ndikuwona ngati kuti za bo. -Mmh! Tulo likumafika nsanga. Basi, mukhale phee! -Nthawi yino timve zolengeza. -Za mu radio. [Kusanzira nkhani za pa radio.] Maliro a Bingu adatayidwa kale. Adzatayidwa m'mawa, kwa Namasalima, kwa T.A. Malemia. A Joyce Bwanali. Unamvapo awatchula tsiku limelo a Joyce Bwanali? Anamwalira dzulo. Kwa Mkwamba. Kwa Bwanali komweko. Tsopano mumvera nkhani za m'maboma... ...atakupatsileni ndi a Chibade. Iwe Edith ukuku, kaya wakutiko, kaya wa kwa Mkwamba wayambanso kuphika zibade. Wabigili yokhala ngati ya kwa Fanny ija. -Ya green? -Eeh! Imene ija ndiyakwa ujeni... -Yakwa ndani? -Amagilasi, si amayi? -Ee. -Mmalo mwa Bessy kwabwera wantchito. -Amene aja? -Eeh. Ellete lero wandipatsa chimwamwasa. Ine kummana zana lija ndinakugayila ndasi kwa Zione. Ine nde ndangomuwuza apongo angatu amenewa. Apongo anga eya. Mumangoziyamba za chipongo chifukwa wina ali ndi zokudya. Mwina atati tiziti, iiih apongo tigayireninso. Chipongo chimayambira pamenepo.

